Ezra 10:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthu ali panoŵa ngambiri, ndipo mvula ikugwa kwamphamvu, sitingathe kukaima pa mtetete. Chinanso nchakuti ntchitoyi si ya tsiku limodzi kapena masiku aŵiri, pakuti tidachimwa kwambiri pa nkhani imeneyi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anthu ndiwo ambiri, ndi nyengo yino nja mvula, tilibenso mphamvu yakuima pabwalo, ndi ntchitoyi sindiyo ya tsiku limodzi kapena awiri; pakuti tachulukitsa kulakwa kwathu pa chinthu ichi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma pano pali anthu ambiri ndiponso mvula ikugwa kwambiri, choncho sitingakayime panja. Ndiponso ntchitoyi si ya tsiku limodzi kapena awiri, chifukwa tachimwa kwambiri pa zimene tachitazi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anthu ndiwo ambiri, ndi nyengo yino nja mvula, tiribenso mphamvu yakuima pabwalo, ndi nchitoyi sindiyo ya tsiku limodzi kapena awiri; pakuti tacurukitsa kulakwa kwathu pa cinthu ici.