Ezra 10:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono atsogoleri athu aimirire m'malo mwa msonkhano wonse. Anthu onse a m'mizinda yathu amene adakwatira akazi achilendo abwere pa nthaŵi imene inu munene, ndipo abwere pamodzi ndi akulu ndi aweruzi a mzinda uliwonse. Motero mkwiyo woopsa wa Mulungu wathu pa nkhani imeneyi udzachoka.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ayang'anire ichi tsono akalonga athu a msonkhano wonse, ndi onse a m'midzi mwathu amene anadzitengera akazi achilendo abwere pa nthawi zoikika, ndi pamodzi nao akulu a mudzi wao uliwonse, ndi oweruza ake, mpaka udzatichokera mkwiyo waukali wa Mulungu wathu chifukwa cha mlandu uwu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono mulole kuti atsogoleri athu ayimirire mʼmalo mwa anthu onse. Aliyense wa mʼmizinda yathu amene anakwatira mkazi wachikunja abwere pa nthawi imene inu munene, ndipo abwere pamodzi ndi akuluakulu ndi oweruza a mzindawo. Choncho mkwiyo wa Mulungu wathu udzatichoka.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ayang'anire ici tsono akalonga athu a msonkhano wonse, ndi onse a m'midzi mwathu amene anadzitengera akazi acilendo abwere pa nthawi zoikika, ndi pamodzi nao akuru a mudzi wao uli wonse, ndi oweruza ace, mpaka udzaticokera mkwiyo waukali wa Mulungu wathu cifukwa ca mlandu uwu.