Ezra 10:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho anthu obwerako ku ukapolo aja, adachitadi momwemo. Wansembe Ezara adasankha anthu, akulu a mabanja potsata mafuko ao, aliyense kuchita kumlemba dzina. Pa tsiku loyamba la mwezi wakhumi, adayambapo kuifufuza nkhani imeneyi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anthu otengedwa ndende anachita chotero. Ndi Ezara wansembe, ndi anthu akulu a nyumba za makolo, monga mwa nyumba za makolo ao, iwo onse otchulidwa maina ao, anasankhidwa, nakhala pansi tsiku loyamba la mwezi wakhumi kufunsa za mlanduwu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anthu obwerako ku ukapolo aja anachita zimene zimafunika. Ndipo wansembe Ezara anasankha amuna amene anali atsogoleri a mabanja potsata mafuko awo ndipo onsewo analembedwa mayina awo. Tsiku loyamba la mwezi wa khumi anayambapo kuyifufuza nkhani imeneyi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anthu otengedwa ndende anacita cotero. Ndi Ezara wansembe, ndi anthu akuru a nyumba za makolo, monga mwa nyumba za makolo ao, iwo onse ochulidwa maina ao anasankhidwa, nakhala pansi tsiku loyamba la mwezi wakhumi kufunsa za mlanduwu.