Ezra 10:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tiyeni tsono tichite naye chipangano Mulungu wathu, kuti ifeyo tilekane nawo akazi ameneŵa pamodzi ndi ana ao, potsata uphungu wa inu mbuyanga ndi wa anthu amene amaopa malamulo a Mulungu wathu. Ndipo tidzazichitadi potsata malamulowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsono tipangane ndi Mulungu wathu kuchotsa akazi onse, ndi obadwa mwa iwo, monga mwa uphungu wa mbuye wanga, ndi wa iwo akunjenjemera pa lamulo la Mulungu wathu; ndipo chichitike monga mwa chilamulo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano tiyeni tichite naye pangano Mulungu wathu, kuti tichotse akazi onsewa ndi ana awo, potsata malangizo a inu mbuye wanga ndi wa anthu amene amaopa malamulo a Mulungu wathu. Lolani kuti zichitike motsatira malamulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsono tipangane ndi Mulungu wathu kucotsa akazi onse, ndi obadwa mwa iwo, monga mwa uphungu wa mbuye wanga, ndi wa iwo akunjenjemera pa lamulo la Mulungu wathu; ndipo cicitike monga mwa cilamulo.