Ezra 10:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho Ezara adanyamuka ndipo adalumbiritsa akulu a ansembe, Alevi ndi Aisraele onse, kuti adzachitedi monga m'mene Sekaniya adaanenera. Tsono onsewo adalumbira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanyamuka Ezara, nalumbiritsa akulu a ansembe, ndi Alevi, ndi Aisraele onse, kuti adzachita monga mwa mau awa. Nalumbira iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho Ezara anayimirira ndipo analumbiritsa akulu a ansembe, Alevi ndi Aisraeli onse, kuti adzachitedi monga Sekaniya ananenera. Tsono onse analumbira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanyamuka Ezara, nalumbiritsa akulu a ansembe, ndi Alevi, ndi Aisrayeli onse, kuti adzacita monga mwa mau awa. Nalumbira iwo.