Ezra 10:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Ezara adachokako ku Nyumba ya Mulungu napita ku chipinda cha Yehohanani, mwana wa Eliyasibu, kumene adakachezera usikuwo. Sadadye buledi kapena kumwa madzi. Nthaŵi yonseyo adakhalira kulira chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu obwerako ku ukapolo aja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Ezara ananyamuka pakhomo pa nyumba ya Mulungu, nalowa m'chipinda cha Yehohanani mwana wa Eliyasibu, ndipo atafikako sanadye mkate, sanamwe madzi; pakuti anachita maliro chifukwa cha kulakwa kwa iwo otengedwa ndende.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ezara anachoka ku Nyumba ya Mulungu napita ku chipinda cha Yehohanani, mwana wa Eliyasibu. Anatandala kumeneko usiku wonse ndipo sanadye chakudya kapena kumwa madzi popeza ankalira chifukwa cha kusankhulupirika kwa anthu obwera ku ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Ezara ananyamuka pakhomo pa nyumba ya. Mulungu, nalowa m'cipinda ca Yehohanana mwana wa Eliyasibu, ndipo atafikako sanadya mkate, sanamwa madzi; pakuti anacita maliro cifukwa ca kulakwa kwa iwo otengedwa ndende.