Ezra 10:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adanena kuti, “Wina aliyense akapanda kufika asanathe masiku atatu, ndiye kuti potsata lamulo la atsogoleri ndi la akulu, adzayenera kumlanda katundu wake yense, ndipo adzachotsedwe m'gulu la anthu obwerako ku ukapolo aja.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kuti aliyense wosafikako atapita masiku atatu, monga mwa uphungu wa akalonga ndi akulu, chuma chake chonse chidzaonongeka konse, ndipo iye adzachotsedwa kumsonkhano wa iwo otengedwa ndende.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ananena kuti wina aliyense amene saonekera pakutha pa masiku atatu, adzalandidwa katundu wake, potsata malangizo a nduna ndi akuluakulu, ndipo adzachotsedwa mʼgulu la anthu obwerako ku ukapolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kuti ali yense wosafikako atapita masiku atatu, monga mwa uphungu wa akalonga ndi akuru, cuma cace conse cidzaonongeka konse, ndipo iye adzacotsedwa ku msonkhano wa iwo otengedwa ndende.