Ezra 10:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho anthu onse a m'dziko la Yuda ndi a m'dziko la Benjamini adasonkhana ku Yerusalemu asanathe masiku atatu. Limeneli linali tsiku la 20 la mwezi wachisanu ndi chinai. Ndipo anthu onse adakhala pansi pa bwalo la Nyumba ya Mulungu, ali njenjenje chifukwa cha nkhani imeneyi ndiponso chifukwa cha mvula yambiri imene inkagwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu amuna onse a Yuda ndi Benjamini asanapite masiku atatu, ndiwo mwezi wachisanu ndi chinai, tsiku la makumi awiri a mwezi; nakhala pansi anthu onse m'khwalala pakhomo pa nyumba ya Mulungu, alikunjenjemera chifukwa cha mlandu uwu, ndi chifukwa cha mvulayi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho anthu onse a mʼdziko la Yuda ndi a mʼdziko la Benjamini anasonkhana ku Yerusalemu asanathe masiku atatu. Limeneli linali tsiku la 20 la mwezi wa 9. Anthu onse anakhala pansi pa bwalo la Nyumba ya Mulungu akunjenjemera chifukwa cha mvula yambiri imene inagwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu amuna onse a Yuda ndi Benjamini asanapite masiku atatu, ndiwo mwezi wacisanu ndi cinai, tsiku la makumi awiri a mwezi; nakhala pansi anthu onse m'khwalala pakhomo pa nyumba ya Mulungu, alikunjenjemera cifukwa ca mlandu uwu, ndi cifukwa ca mvulayi.