Ezra 2:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Naŵa anthu a m'chigawo cha Yuda amene adabwerako ku ukapolo, omwe Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adaaŵagwira nkupita nawo ku ukapolo ku Babiloni. Anthuwo adabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wa makolo ake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ana a deralo, amene anakwera kutuluka m'ndende mwa andende aja Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adawatenga ndende kunka nao ku Babiloni, nabwerera kunka ku Yerusalemu ndi Yuda, yense kumudzi wake, ndi awa:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Awa ndi anthu a mʼchigawo cha Yuda amene anabwerako ku ukapolo, amene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anawagwira ukapolo ndi kupita nawo ku Babuloni (iwo anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense ku mzinda wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ana a deralo, amene anakwera kuturuka m'ndende mwa andende aja Nebukadinezara mfumu ya Babulo adawatenga ndende kumka nao ku Babulo, nabwerera kumka ku Yerusalemu ndi Yuda, yense ku mudzi wace, ndi awa: