Ezra 2:59 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu ali m'munsiŵa ndiwo amene adabwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adani ndi ku Imeri, ngakhale sankatha kutsimikiza kuti makolo ao kapena mafuko ao analidi Aisraele enieni kapena ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo okwera kuchokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adani, Imeri, ndi awa, koma sanakhoze kutchula nyumba za makolo ao ndi mbumba zao ngati ali Aisraele:
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ali mʼmunsiwa anabwera kuchokera ku mizinda ya Teli-Mela, Teli-Harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, ngakhale samatha kutsimikiza kuti mafuko awo analidi Aisraeli enieni kapena ayi:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo okwera kucokera ku Telemela, Teleharisa, Kerubi, Adana, Imeri, ndi awa, koma sanakhoza kuchula nyumba za makolo ao ndi mbumba zao ngati ali Aisrayeli: