Ezra 2:61 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiponso ena mwa ansembe anali aŵa: a banja la Habaya, a banja la Hakozi ndi a banja la Barizilai (kunena amene adaakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi, nkutenga dzina la bambo waoyo).
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi ana a ansembe: ana a Habaya, ana a Hakozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgiliyadi, natchedwa dzina lao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndi ena pakati pa ansembe anali awa: Zidzukulu za Hobiya, Hakozi, ndi Barizilai (Zidzukulu za Hobiya, zidzukulu za Hakozi ndi zidzukulu za Barizilai. Barizilai ameneyu ndi uja anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Barizilai Mgiliyadi ndipo ankadziwika ndi dzina la bambo wawoyo.)
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ana a ansembe: ana a Habaya, ana a Kozi, ana a Barizilai, amene anadzitengera mkazi wa ana akazi a Barizilai Mgileadi, nachedwa dzina lao.