Ezra 2:68 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene adabwera ku Nyumba ya Chauta ku Yerusalemu, atsogoleri ena a mabanja adapereka mphatso zaufulu, kuperekera Nyumba ya Mulungu, kuti imangidwenso pamalo pake pakale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akulu ena a nyumba za makolo, pofika kunyumba ya Yehova ili ku Yerusalemu, anapereka chaufulu kwa nyumba ya Mulungu chakuiimika pakuzika pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atafika ku Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu, ena mwa atsogoleri a mabanja anapereka zopereka zaufulu zothandizira kumanganso Nyumba ya Mulungu pamalo pake pakale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akulu ena a nyumba za makolo, pofika ku nyumba ya Yehova iri ku Yerusalemu, anapereka caufulu kwa nyumba ya Mulungu cakulimika pakuzika pace.