Ezra 3:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono amisiri omanga nyumba atamanga maziko a Nyumba ya Chauta, ansembe adadza akuimba malipenga atavala zovala zaunsembe. Ndipo Alevi, zidzukulu za Asafu, adadza akuimba ziwaya zamalipenga ndi kutamanda Chauta, potsata malangizo a Davide mfumu ya Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pomanga maziko a Kachisi wa Yehova, amisiriwo anaimiritsa ansembe ovala zovala zao ndi mphalasa, ndi Alevi ana a Asafu ndi nsanje, kuti alemekeze Yehova, monga umo anaikiratu Davide mfumu ya Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amisiri omanga nyumba atamanga maziko a Nyumba ya Yehova, ansembe anabwera akuyimba malipenga, atavala zovala zaunsembe. Ndipo Alevi, zidzukulu za Asafu, anadza akuyimba matambolini ndi kutenga udindo wawo wotamanda Yehova, potsata malangizo a Davide mfumu ya Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pomanga maziko a Kacisi wa Yehova, amisiriwo anaimiritsa ansembe obvala zobvala zao ndi mphalasa, ndi Alevi ana a Asafu ndi nsanje, kuti alemekeze Yehova, monga umo anaikiratu Davide mfumu ya Israyeli.