Ezra 3:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma ambiri mwa ansembe, Alevi ndi atsogoleri a mabanja, ndiponso nkhalamba zimene zidaaona nyumba yoyamba, adalira mokweza mau, ataona maziko a nyumba imeneyi akumangidwa. Komabe ambirinso ankafuula mokondwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ansembe ambiri, ndi Alevi, ndi akulu a nyumba za makolo, okalamba amene adaona nyumba yoyamba ija, pomanga maziko a nyumba iyi pamaso pao, analira ndi mau akulu; koma ambiri anafuulitsa mokondwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ambiri mwa ansembe, Alevi ndiponso atsogoleri amabanja, akuluakulu amene anaona Nyumba ya Yehova yakale, analira mokweza pamene anaona maziko a nyumbayi akumangidwa. Komanso ena ambiri ankafuwula mosangalala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ansembe ambiri, ndi Alevi, ndi akuru a nyumba za makolo, okalamba amene adaona nyumba yoyamba ija, pomanga maziko a nyumba iyi pamaso pao, analira ndi mau akuru; koma ambiri anapfuulitsa mokondwera.