Ezra 3:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho anthu sankatha kusiyanitsa liwu lofuula mokondwerera ndi liwu la anthu olira, popeza kuti anthuwo ankafuula kwambiri ndipo liwu la kufuulako linkamveka kutali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Potero anthu sanazindikire phokoso la kufuula mokondwera kulisiyanitsa ndi phokoso la kulira kwa anthu; pakuti anthu anafuulitsa kwakukulu, ndi phokoso lake lidamveka kutali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho panalibe amene ankatha kusiyanitsa liwu lofuwula mokondwerera ndi liwu la anthu olira, chifukwa anthuwo ankafuwula kwambiri. Ndipo liwu lofuwulalo limamveka kutali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Potero anthu sanazindikira phokoso la kupfuula mokondwera kulisiyanitsa ndi phokoso la kulira kwa anthu; pakuti anthu anapfuulitsa kwakukuru, ndi phokoso lace lidamveka kutari.