Ezra 3:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Yesuwa, mwana wa Zadoki, ndi ansembe anzake, pamodzi ndi Zerubabele, mwana wa Sealatiele, ndi abale ake, adayamba kumanga guwa la Mulungu wa Aisraele. Adafuna kuti aziperekapo nsembe zopsereza, monga adalembera m'buku la malamulo a Mose, munthu wa Mulungu uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanyamuka Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ake ansembe, ndi Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi abale ake, namanga guwa la nsembe la Mulungu wa Israele, kuperekapo nsembe zopsereza, monga mulembedwa m'chilamulo cha Mose munthu wa Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yesuwa mwana wa Yozadaki ndi ansembe anzake pamodzi ndi Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi abale ake anayamba kumanga guwa lansembe la Mulungu wa Israeli. Anatero pofuna kuti aziperekapo nsembe zopsereza monga analembera mʼbuku la Mose, munthu wa Mulungu uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanyamuka Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ace ansembe, ndi Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ndi abale ace, namanga guwa la nsembe la Mulungu wa Israyeli, kuperekapo nsembe zopsereza, monga mulembedwa m'cilamulo ca Mose munthu wa Mulungu.