Ezra 3:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe kudalembedwera. Masiku onse ankaperekanso nsembe zopsereza potsata chiŵerengero chake chofunika tsiku ndi tsiku, monga kudalembedwera.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nachita chikondwerero cha Misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ake, monga mwa lamulo lake la tsiku lake pa tsiku lake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ankasunga tsiku la chikondwerero cha misasa monga momwe zinalembedwera. Ankaperekanso nsembe za tsiku ndi tsiku monga mwa chiwerengero chake potsata mwambo wake wa tsiku ndi tsiku monga zinalembedwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nacita madyerero a misasa monga kwalembedwa, napereka nsembe yopsereza tsiku ndi tsiku mawerengedwe ace, monga mwa lamulo lace la tsiku lace pa tsiku lace;