Ezra 3:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanunchiŵiri, adayamba kupereka nsembe zopserezazi kwa Chauta. Koma maziko a Nyumba ya Mulungu anali asanamangidwebe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chiyambire tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova; koma sanamange maziko a Kachisi wa Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiwiri, iwo anayambanso kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova, ngakhale kuti maziko a Nyumba ya Yehova anali asanamangidwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ciyambire tsiku loyamba la mwezi wacisanu ndi ciwiri anapereka nsembe zopsereza kwa Yehova; koma sanamange maziko a Kacisi wa Yehova.