Ezra 3:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono anthu adapereka ndalama kwa amisiri osema miyala ndi kwa amisiri a matabwa. Adatumiza chakudya, zakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi ku Tiro, kuti azigulira mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni. Mitengoyo adafika nayo ku nyanja mpaka ku mzinda wa Yopa. Zonsezi ankazichita potsata chilolezo cha Kirusi, mfumu ya ku Persiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anaperekanso ndalama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi chakudya, ndi chakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Tiro, kuti atenge mikungudza ku Lebanoni, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Kirusi mfumu ya Persiya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo anapereka ndalama kwa amisiri a miyala ndi kwa amisiri a matabwa, ndi chakudya, chakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi a ku Turo, kuti abweretse mitengo ya mkungudza pa nyanja kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Yopa. Zonsezi anachita malinga ndi chilolezo chimene analandira kuchokera kwa Koresi, mfumu ya Peresiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anaperekanso ndarama kwa amisiri a miyala, ndi a mitengo; ndi cakudya, ndi cakumwa, ndi mafuta, kwa a ku Sidoni, ndi a ku Turo, kuti atenge mikungudza ku Lebano, kufika nayo ku nyanja ku Yopa, monga adawalola Koresi mfumu ya Babulo.