Ezra 3:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yesuwa ndi ana ake kudzanso achibale ake, ndiponso Kadimiyele ndi ana ake, ana a Yuda, onsewo pamodzi adasenza udindo woyang'anira anthu antchito ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo ana a Henadadi, ndiponso Alevi ndi ana ao ndi achibale ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anaimirira pamodzi Yesuwa ndi ana ake ndi abale ake, Kadimiyele ndi ana ake, ana a Yuda, kuyang'anira ogwira ntchito m'nyumba ya Yehova, ana a Henadadi ndi ana ao ndi abale ao Alevi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yesuwa ndi ana ake aamuna kudzanso abale ake, Kadimieli ndi ana ake (ana a Yuda) onse pamodzi anasenza udindo woyangʼanira antchito ku Nyumba ya Mulungu, kuphatikizanso ana a Henadadi komanso Alevi, ana awo ndi abale awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anaimirira pamodzi Yesuwa ndi ana ace ndi abale ace, Kadimiyeli ndi ana ace, ana a Yuda, kuyang'anira ogwira nchito m'nyumba ya Yehova, ana a Henadadi ndi ana ao ndi abale ao Alevi.