Ezra 4:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Amfumu, tikuti mudziŵeko kuti Ayuda omwe adabwera kuno kuchokera kwanuko, apita ku Yerusalemu. Akumanganso mzinda wopanduka ndi woipa uja. Akumaliza makoma ake ndipo akukonza maziko.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adziwe mfumu kuti, Ayuda adakwerawo ochokera kwanu atifikira ife ku Yerusalemu, alikumanga mudzi uja wopanduka ndi woipa, alikutsiriza malinga ake, nalumikiza maziko ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amfumu tati mudziwe kuti Ayuda amene anabwera kuno kuchokera kwanuko apita ku Yerusalemu ndipo akumanganso mzinda wa anthu owukira ndi oyipa uja. Akumaliza makoma ake ndipo akukonzanso maziko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adziwe mfumu kuti, Ayuda adakwerawo ocokera kwanu atifikira ife ku Yerusalemu, alikumanga mudzi uja wopanduka ndi woipa, alikutsiriza malinga ace, nalumikiza maziko ace.