Ezra 4:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsonotu amfumu, mudziŵe kuti akaumanganso mzinda umenewu ndi kumaliza kumanga makoma ake, ndiye kuti anthu aja adzaleka kukhoma msonkho ndi kupereka kasitomo kapena msonkho wa kanthu kena kalikonse, ndipo chuma choloŵa m'thumba la mfumu chidzachepa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adziwe tsono mfumu, kuti akamanga mudzi uwu ndi kutsiriza malinga ake, sadzapereka msonkho, kapena thangata, kapena msonkho wa m'njira; ndipo potsiriza pake kudzasowetsa mafumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuwonjeza apo amfumu mudziwe kuti ngati amalize kumanganso mzindawu ndi kukonzanso makoma ake, adzaleka kukhoma msonkho, kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko kapena msonkho wina uliwonse, ndipo chuma cha thumba la ufumu chidzachepa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adziwe tsono mfumu, kuti akamanga mudzi uwu ndi kutsiriza malinga ace, sadzapereka msonkho, kapena thangata, kapena msonkho wa m'njira; ndipo potsiriza pace kudzasowetsa mafumu.