Ezra 4:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono popeza kuti ife ndife akadyere kwa mfumu, si bwino kuti tizingopenya zinthu zochititsa mfumu manyazi. Nchifukwa chake tikutumiza mau kwa inu mfumu kuti mudziŵe zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza tsono timadya mchere wa m'nyumba ya mfumu, sitiyenera kungopenyerera mpepulo wa pa mfumu; chifukwa chake tatumiza ndi kudziwitsa mfumu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza tsono ife timadya nawo kwa mfumu sitiyenera tizingoonerera zinthu zochititsa mfumu manyazi. Nʼchifukwa chake tikutumiza uthenga kwa inu a mfumu kuti mudziwe zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza tsono timadya mcere wa m'nyumba ya mfumu, sitiyenera kungopenyerera mpepulo wa pa mfumu; cifukwa cace tatumiza ndi kudziwitsa mfumu,