Ezra 4:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndi bwino kuti pachitike kafukufuku m'buku la mbiri yakale ya makolo anu. M'buku lazakalemo mudzapeza ndi kuŵerengamo kuti mzinda umenewo ndi waupandu, wosautsa mafumu ndi nduna zam'madera zomwe. Kuyambira kale wakhala ukuchita zoukira ulamuliro uliwonse. Nchifukwa chake mzinda umene uja adausandutsa bwinja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti afunefune m'buku la chikumbutso la makolo anu; momwemo mudzapeza m'buku la chikumbutso, ndi kudziwa kuti mudzi uwu ndi mudzi wopanduka, ndi wosowetsa mafumu, ndi maiko; ndi kuti amadziyendera m'menemo kuyambira kale lomwe; ndicho chifukwa chakuti anapasula mudzi uwu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho pachitike kafukufuku mʼbuku la mbiri yakale ya makolo anu. Mʼbuku la mbiri zakale mudzapezamo ndi kuwerenga kuti mzinda umenewu ndi waupandu, wosautsa mafumu ndi nduna zamʼmadera zomwe. Kuyambira kale wakhala ukuwukira ulamuliro uliwonse. Nʼchifukwa chake mzinda umenewu anawuwononga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti afunefune m'buku la cikumbutso la makolo anu; momwemo mudzapeza m'buku la cikumbutso, ndi kudziwa kuti mudzi uwu ndi mudzi wopanduka, ndi wosowetsa mafumu, ndi maiko; ndi kuti amadziyendera m'menemo kuyambira kale lomwe; ndico cifukwa cakuti anapasula mudzi uwu.