Ezra 4:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tikukudziŵitsani inu amfumu kuti ngati mzinda umenewu aumanganso ndi kutsirizanso makoma ake, ndiye kuti inuyo simudzatha kumalamulirabe m'chigawo cha Patsidya pa Yufuratecho.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tili kudziwitsa mfumu kuti ukamangidwa mudziwu, nakatsirizidwa malinga ake, simudzakhala nalo gawo tsidya lino la mtsinjewo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono tikukudziwitsani amfumu kuti ngati mzinda umenewu umangidwanso ndi makoma ake nʼkutsirizidwanso ndiye kuti inu simudzalamuliranso chigawo cha patsidya pa Yufurate.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tirikudziwitsa mfumu kuti ukamangidwa mudziwu, nakatsirizidwa malinga ace, simudzakhala nalo gawo tsidya lino la mtsinjewo.