Ezra 4:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mfumuyo idayankha kalatayo motere, “Bwanamkubwa Rehumu ndi mlembi Simisai, ndi anzanu ena amene akukhala ku Samariya ndi m'chigawo cha Patsidya pa Yufurate, ndikuti moni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mfumu nibweza mau kwa Rehumu chiwinda cha malamulo, ndi kwa Simisai mlembi, ndi kwa anzao otsala okhala m'Samariya, ndi otsala tsidya lino la mtsinjewo, Mtendere, ndi nthawi yakuti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inatumiza yankho ili: Mkulu wa gulu lankhondo Rehumu, mlembi Simisai ndi anzanu onse amene akukhala ku Samariya ndi mʼzigawo zina zonse za Patsidya pa Yufurate. Landirani moni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mfumu nibweza mau kwa Rehumu ciwinda ca malamulo, ndi kwa Simsai mlembi, ndi kwa anzao otsala okhala m'Samariya, ndi otsala tsidya lino la mtsinjewo, Mtendere, ndi nthawi yakuti.