Ezra 4:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine nditalamula kuti afufuzefufuze nkhaniyi, kwapezekadi kuti mzinda umenewo udaaukira mafumu kale, ndipo kuti zaupandu ndi zoukira zinkachitikadi m'menemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndinalamulira anthu, nafunafuna, napeza kuti mudzi uwu unaukira mafumu kuyambira kale lomwe, ndi kuti akachitamo mpanduko ndi kudziyendera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine nditalamula kuti afufuze nkhaniyi kwapezekadi kuti mzinda umenewu uli ndi mbiri yowukira mafumu ndi kuti zaupandu ndi zowukira zinkachitikadi mʼmenemo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndinalamulira anthu, nafunafuna, napeza kuti mudzi uwu unaukira mafumu kuyambira kale lomwe ndi kuti akacitamo mpanduko ndi kudziyendera.