Ezra 4:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye adadza kwa Zerubabele ndi kwa atsogoleri a mabanja, naŵauza kuti, “Mutilole kuti timange nawo, pakuti ife timapembedza Mulungu wanu monga momwe mumachitira inu, ndipo takhala tikupereka nsembe kwa Iye kuyambira nthaŵi ya Ezaradoni, mfumu ya ku Asiriya, amene adatifikitsa kuno.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
anayandikira kwa Zerubabele, ndi kwa akulu a nyumba za makolo, nanena nao, Timange pamodzi nanu; pakuti timfuna Mulungu wanu monga inu, ndipo timamphera nsembe chiyambire masiku a Esarahadoni mfumu ya Asiriya, amene anatikweretsa kuno.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono anapita kwa Zerubabeli ndi kwa atsogoleri a mabanja awo ndi kunena kuti, “Mutilole kuti tikuthandizeni kumangaku chifukwa ife timapembedza Mulungu wanu monga momwe mumachitira inu, ndipo takhala tikupereka nsembe kwa Iye kuyambira nthawi ya Esrahadoni, mfumu ya ku Asiriya, amene anabwera nafe kuno.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
anayandikira kwa Zerubabele, ndi kwa akulu a nyumba za makolo, nanena nao, Timange pamodzi nanu; pakuti timfuna Mulungu wanu monga inu, ndipo timamphera nsembe ciyambire masiku a Ezaradoni mfumu ya Asuri, amene anatikweretsa kuno.