Ezra 4:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mafumu amphamvu adakhala akulamulira Yerusalemu ndi chigawo chonsecho cha Patsidya pa Yufurate, namalandira kasitomo ndi msonkho pa kanthu kena kalikonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Panalinso mafumu amphamvu m'Yerusalemu amene anachita ufumu tsidya lija lonse la mtsinje, ndipo anthu anawapatsa msonkho, thangata, ndi msonkho wa m'njira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mafumu amphamvu akhala akulamulira Yerusalemu ndi chigawo chonse cha Patsidya pa Yufurate. Iwo ankalandira msonkho ndi kulipira ndalama zakatundu olowa mʼdziko pa kanthu kena kalikonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Panalinso mafumu amphamvu m'Yerusalemu amene anacita ufumu tsidya lija lonse la mtsinje, ndipo anthu anawapatsa msonkho, thangata, ndi msonkho wa m'njira.