Ezra 4:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono inu mulembe lamulo loŵaletsa anthu amenewo kuti asamangenso mzinda umenewo, mpaka ine nditaloleza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mulamulire tsono kuti anthu awa aleke, ndi kuti asamange mudzi uwu, mpaka ndidzalamulira ndine.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano inu khazikitsani lamulo kuti anthu amenewo asiye ntchitoyo, asamangenso mzindawo mpaka ine nditalamula
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mulamulire tsono kuti anthu awa aleke, ndi kuti asamange mudzi uwu, mpaka ndidzalamulira ndine.