Ezra 4:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kalata ya mfumu Arita-kisereksesiyo ataiŵerenga pamaso pa Rehumu ndi mlembi Simisai ndi anzao, iwowo adapita msangamsanga ku Yerusalemu, nakaŵaletsa Ayuda aja mwamphamvu kuti asapitirize ntchito yao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo atawerenga malemba a kalata wa mfumu Arita-kisereksesi kwa Rehumu, ndi Simisai mlembi, ndi anzao, anafulumira kupita ku Yerusalemu kwa Ayuda, nawaletsa ndi dzanja lamphamvu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kalata ya mfumu Aritasasitayi itangowerengedwa pamaso pa Rehumu ndi Simisai mlembi uja, ndi anzawo onse, iwo anapita msangamsanga ku Yerusalemu kukawaletsa Ayuda aja mwamphamvu kuti asapitirire ntchito yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo atawerenga malemba a kalata wa mfumu kwa Rehumu, ndi Simsai mlembi, ndi anzao, anafulumira kupita ku Yerusalemu kwa Ayuda, nawaletsa ndi dzanja lamphamvu.