Ezra 5:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo adatiyankha kuti, ‘Ife ndife atumiki a Mulungu wa dziko lakumwamba ndi wa dziko lapansi, ndipo tikumanganso Nyumba imene mfumu ina yamphamvu ya Israele idaamanga ndi kuimaliza zaka zamakedzana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Natiyankha mau motere, ndi kuti, Ife ndife akapolo a Mulungu wa Kumwamba ndi dziko lapansi, tilikumanga nyumba imene idamangika zapita zaka zambiri; inaimanga ndi kuitsiriza mfumu yaikulu ya Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yankho limene anatipatsa ndi ili: “Ife ndife atumiki a Mulungu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi, ndipo tikumanganso Nyumba imene mfumu ina yamphamvu ya Israeli inamanga ndi kuyitsiriza zaka zambiri zapitazo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Natiyankha mau motere, ndi kuti, Ife ndife akapolo a Mulungu wa Kumwamba ndi dziko lapansi, tirikumanga nyumba imene idamangika zapita zaka zambiri; inaimanga ndi kuitsiriza mfumu yaikuru ya Israyeli.