Ezra 5:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma chifukwa choti makolo athu adaakwiyitsa Mulungu Wakumwamba, Iye adaaŵapereka kwa Nebukadinezara, Mkaldea, mfumu ya ku Babiloni. Ndiye amene adaaononga nyumba ino, natenga anthu onse kunka nawo ku ukapolo ku Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma makolo athuwo atautsa mkwiyo wa Mulungu wa Kumwamba, Iye anawapereka m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni Mkaldeya, amene anaononga nyumba yino, natenga anthu ndende kunka nao ku Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma chifukwa chakuti makolo athu anakwiyitsa Mulungu wakumwamba, Iye anawapereka kwa Nebukadinezara Mkalideya, mfumu ya Babuloni, amene anawononga Nyumbayi ndi kutenga anthu onse kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma makolo athuwo atautsa mkwiyo wa Mulungu wa Kumwamba, Iye anawapereka m'dzanja la Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo Mkasidi, amene anaononga nyumba yino, natenga anthu ndende kumka nao ku Babulo.