Ezra 5:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo ziŵiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara adaatulutsa ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ndi kukazilonga m'nyumba ya milungu ya ku Babiloni, zomwezonso mfumu Kirusiyo adazitulutsa ku nyumba ya milungu ya ku Babiloniyo, nazitumiza kwa munthu wina dzina lake Sesibazara, amene mfumu idampatsa ulamuliro mu Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndiponso zipangizo za golide ndi siliva za nyumba ya Mulungu, anazitulutsa Nebukadinezara m'Kachisi anali ku Yerusalemu, ndi kubwera nazo ku Kachisi wa ku Babiloni, izizo Kirusi mfumu anazitulutsa m'Kachisi wa ku Babiloni, nazipereka kwa munthu dzina lake Sezibazara, amene anamuika akhale kazembe;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anazitenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ndi kukaziyika mʼnyumba ya milungu ya ku Babuloni, anakazichotsa ku nyumba ya milungu ya ku Babuloniko ndi kuzipereka kwa Sesibazara, amene mfumu inamusankha kukhala bwanamkubwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndiponso zipangizo za golidi ndi siliva za nyumba ya Mulungu, anaziturutsa Nebukadinezara m'Kacisi anali ku Yerusalemu, ndi kubwera nazo ku kacisi wa ku Babulo, izizo Koresi mfumu anaziturutsa m'kacisi wa ku Babulo, nazipereka kwa munthu dzina lace Sezibazara, amene anamuika akhale kazembe;