Ezra 5:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake tsono, chikakukomerani inu mfumu, pachitike kafukufuku m'nyumba mosungira chuma ndi mabuku okhudza mbiri zakale ku Babiloniko, kuti tiwone ngati mfumu Kirusi adaaperekadi lamulo lonena za kumanganso Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Kenaka chonde, inu amfumu, mutidziŵitse zomwe zikukondwetseni kuti mugamule pa nkhani imeneyi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsono chikakomera mfumu, munthu asanthule m'nyumba ya chuma cha mfumu ili komwe ku Babiloni, ngati nkuterodi, kuti Kirusi mfumu analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu ku Yerusalemu; ndipo mfumu ititumizire mau omkomera pa chinthuchi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake ngati chingakukomereni amfumu, pachitike kafukufuku mʼnyumba yaufumu mosungira chuma ndi mabuku okhudza mbiri ya Babuloni kuti tione ngati mfumu Koresi inalamuladi za kumanganso Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Kenaka amfumu mutiwuze zomwe zikukondweretsani kuti mugamule pa nkhani imeneyi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsono cikakomera mfumu, munthu asanthule m'nyumba ya cuma ca mfumu iri komwe ku Babulo, ngati nkuterodi, kuti Koresi mfumu analamulira kuti azimanga nyumba iyi ya Mulungu ku Yerusalemu; ndipo mfumu ititumizire mau omkomera pa cinthuci.