Ezra 5:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamva mauwo, Zerubabele mwana wa Sealatiele ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki adanyamuka nakayambanso kumanga Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Aneneri a Mulunguwo nawonso anali nawo pamodzi namaŵathandiza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake Zerubabeli mwana wa Sealatieli ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki ananyamuka nakayambanso kumanga Nyumba ya Mulungu mu Yerusalemu. Ndipo aneneri a Mulungu anali nawo pamodzi, kuwathandiza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Zerubabele mwana wa Sealitiyeli, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ananyamuka, nayamba kumanga nyumba ya Mulungu iri ku Yerusalemu, anali pamodzi nao aneneri a Mulungu akuwathandiza.