Ezra 5:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi yomweyo Tatenai, bwanamkubwa wa chigawo cha Patsidya pa Yufurate ndi Setari-Bozenai, pamodzi ndi anzao adapita kwa iwowo, ndipo adalankhula nawo naŵafunsa kuti, “Adakulamulani ndani kuti mumange Nyumba imeneyi ndi kumaliza khoma lake?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nthawi yomweyi anawadzera Tatenai kazembe tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setari-Bozenai, ndi anzao, nanena nao motere, Anakulamulirani inu ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi imeneyo Tatenai, bwanamkubwa wa chigawo cha patsidya pa Yufurate pamodzi ndi Setari-Bozenai ndi anzawo anapita kwa iwo ndi kukawafunsa kuti, “Anakulolani ndani kuti mumangenso Nyumba imeneyi ndi kutsiriza khoma lake?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nthawi yomweyi anawadzera Tatinai kazembe tsidya lino la mtsinjewo, ndi Setara Bozinai, ndi anzao, nanena nao motere, Anakulamulirani inu ndani kumanga nyumba iyi, ndi kutsiriza khoma ili?