Ezra 5:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mfumu, mudziŵe kuti ife tidaapita ku dziko la Yuda ku Nyumba ya Mulungu wamkulu. Nyumbayo ikumangidwa ndi miyala ikuluikulu, ndipo akuyalika mitengo pa makoma. Ntchito imeneyi ikuchitika mwachangu, ndipo ikuyenda bwino kwambiri poigwira anthuwo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adziwe mfumu kuti ife tinamuka kudziko la Yuda, kunyumba ya Mulungu wamkulu, yomangidwa ndi miyala yaikulu, niikidwa mitengo pamakoma, nichitika mofulumira ntchitoyi, nikula m'dzanja mwao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Amfumu mudziwe kuti ife tinapita ku dziko la Yuda ku Nyumba ya Mulungu wamkulu. Nyumbayo ikumangidwa ndi miyala ikuluikulu ndipo akuyala matabwa pa makoma. Ntchitoyi ikugwiridwa mwachangu ndipo ikuyenda bwino kwambiri mwautsogoleri wawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adziwe mfumu kuti ife tinamuka ku dziko la Yuda, ku nyumba ya Mulungu wamkuru, yomangidwa ndi miyala yaikuru, niikidwa mitengo pamakoma, nicitika mofulumira nchitoyi, nikula m'dzanja mwao.