Ezra 6:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atalandira mauwo mfumu Dariusi adapanga lamulo ndipo kafukufuku adachitikadi ku Babiloni m'nyumba mosungira chuma ndi mabuku okhudza mbiri zakale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo analamulira Dariusi mfumu, ndipo anthu anafunafuna m'nyumba ya mabuku mosungira chuma m'Babiloni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atalandira mawuwo mfumu Dariyo anapereka lamulo ndipo kafukufuku anachitikadi ku Babuloni mʼnyumba yosungira chuma ndi mabuku ambiri yakale.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo analamulira Dariyo mfumu, ndipo anthu anafunafuna m'nyumba ya mabuku mosungira cuma m'Babulo.