Ezra 6:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndikupanganso lamulo lakuti ngati wina aliyense asintha zimene ndalamulazi, ndiye kuti adzasololako mtanda wa nyumba yake nadzamkhomera pamenepo, ndipo nyumba yakeyo adzaisandutsa dzala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndalamuliranso kuti aliyense adzasintha mau awa, usololedwe mtanda kunyumba kwake, namkweze, nampachike pomwepo; niyesedwa dzala nyumba yake chifukwa cha ichi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndikulamulanso kuti ngati wina asintha zimene ndalamulazi, mtanda umodzi wa nyumba yake udzasololedwa ndi kumunkhomera pamenepo ndipo nyumba yake adzayisandutse dzala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndalamuliranso kuti ali yense adzasintha mau awa, usololedwe mtanda kunyumba kwace, namkweze, nampacike pomwepo; niyesedwe dzala nyumba yace cifukwa ca ici;