Ezra 6:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mulungu amene adasankhula Yerusalemu kuti akhale malo ompembedzerako, achotse mfumu iliyonse kapena anthu amene adzayerekeze kusintha zimenezi kapena kuwononga Nyumba ya Mulungu yakumeneko. Ine Dariusi ndikuika lamuloli, aliyense alitsate mosamala kwambiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo Mulungu wokhalitsa dzina lake komweko agwetse mafumu onse ndi mitundu yonse ya anthu, akutulutsa dzanja lao kusintha mau awa, kuononga nyumba ya Mulungu ili ku Yerusalemu. Ine Dariusi ndalamulira, chichitike msanga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulungu amene anasankha kuti anthu azimupembedza pa malo amenewa, achotse mfumu iliyonse kapena munthu aliyense amene adzasinthe zimenezi kapena kuwononga Nyumba ya Mulungu ya ku Yerusalemuko. Ine Dariyo ndikuyika lamuloli, aliyense alitsate mosamala kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo Mulungu wokhalitsa dzina lace komweko agwetse mafwnu onse ndi mitundu yonse ya anthu, akuturutsa dzanja lao kusintha mau awa, kuononga nyumba ya Mulungu iri ku Yerusalemu. Ine Dariyo ndalamulira, cicitike msanga.