Ezra 6:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo akulu a Ayuda adapititsa m'tsogolo ntchito yomanga ija. Iwo ankalimbikitsidwa ndi aneneri aja Hagai ndi Zekariya mwana wa Ido. Adamaliza ntchito yao yomanga Nyumba, monga momwe Mulungu wa Israele adaalamulira, ndiponso potsata lamulo la Kirusi, la Dariusi, ndi la Arita-kisereksesi, mafumu a ku Persiya.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo akulu a Ayuda anamanga opanda chosoweka, mwa kunenera kwa mneneri Hagai, ndi Zekariya mwana wa Ido. Naimanga, naitsiriza, monga mwa lamulo la Mulungu wa Israele, ndi monga mwa lamulo la Kirusi, ndi Dariusi, ndi Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo akuluakulu a Ayuda anapitiriza ntchito yomanga ija molimbikitsidwa ndi aneneri Hagai ndi Zekariya mwana wa Ido. Anamaliza ntchito yomanga Nyumbayo, monga momwe Mulungu wa Israeli analamulira ndiponso potsata lamulo la Koresi, Dariyo ndi Aritasasita, mafumu a ku Perisiya.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo akulu a Ayuda anamanga opanda cosoweka, mwa kunenera kwa mneneri Hagai, ndi Zekariya mwana wa Ido. Naimanga, naitsiriza, monga mwa lamulo la Mulungu wa Israyeli, ndi monga mwa lamulo la Koresi, ndi Dariyo, ndi Aritasasta mfumu ya Perisiya,