Ezra 6:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pochita mwambo umenewo, anthuwo adapereka nsembe za ng'ombe zamphongo 100, nkhosa zamphongo 200, anaankhosa 400. Adaperekanso atonde khumi ndi aŵiri ngati nsembe yopepesera uchimo wa anthu onse, potsata chiŵerengero cha mafuko a Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo popatulira nyumba iyi ya Mulungu anapereka ng'ombe zana limodzi, nkhosa zamphongo mazana awiri, anaankhosa mazana anai, ndi za nsembe yazolakwa ya Aisraele onse atonde khumi ndi awiri, monga mwa kuwerenga kwake kwa mafuko a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Poporeka Nyumba ya Mulunguyi, anthu anapereka nsembe za ngʼombe zazimuna 100, nkhosa zazimuna 200, ana ankhosa aamuna 400. Anaperekanso mbuzi zazimuna 12 ngati nsembe yopepesera machimo a anthu onse, potsata chiwerengero cha mafuko a Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo popatulira nyumba iyi ya Mulungu anapereka ng'ombe zana limodzi, nkhosa zamphongo mazana awiri, ana a nkhosa mazana anai, ndi za nsembe yazolakwa ya Aisrayeli onse atonde khumi ndi awiri, monga mwa kuwerenga kwace kwa mapfuko a Israyeli.