Ezra 6:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ansembe ndi Alevi anali atadziyeretsa, tsono onsewo anali oyeradi. Choncho adapha mwanawankhosa wa Paska, kuphera onse amene adatuluka ku ukapolo, ansembe anzao ndi eniakewo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ansembe ndi Alevi anadziyeretsa pamodzi, anayera onsewo, naphera Paska chifukwa cha ana onse a ndende, ndi abale ao ansembe, ndi iwo okha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ansembe ndi Alevi anali atadziyeretsa ndipo onsewo anali oyeretsedwa. Alevi anapha mwana wankhosa wa Paska kuphera onse amene anatuluka ku ukapolo, ansembe anzawo ndi iwo eni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ansembe ndi Alevi anadziyeretsa pamodzi, anayera onsewo, naphera Paskha cifukwa ca ana onse a ndende, ndi abale ao ansembe, ndi iwo okha.