Ezra 6:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nkhosa ya Paskayo adaidya Aisraele onse amene adatuluka ku ukapolo. Adadyakonso wina aliyense amene adaphatikana nawo, atadziyeretsa ku zonyansa za mitundu ina ya anthu akunja am'dzikomo, kuti apembedze Chauta, Mulungu wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ana a Israele obwera kundende, ndi yense wakudzipatulira kuchokera chonyansa cha amitundu, kutsata iwowa, kufuna Yehova Mulungu wa Israele, anadza,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nkhosa ya Paskayo anayidya ndi Aisraeli onse amene anatuluka ku ukapolo, wina aliyense amene anaphatikana nawo atadziyeretsa ku zonyansa za mitundu ina ya anthu akunja a mʼdzikomo kuti apembedze Yehova Mulungu wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ana a Israyeli obwera kundende, ndi yense wakudzipatulira kucokera conyansa ca amitundu, kutsata iwowa, kufuna Yehova Mulungu wa Israyeli, anadza,