Ezra 6:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero pa masiku asanu ndi aŵiri adasangalala pa chikondwerero cha buledi wosatupitsa. Zidatero chifukwa Chauta adaŵakondweretsa, ndipo adaatembenuza mtima wa mfumu ya ku Asiriya, kotero kuti idaŵakomera mtima niŵathandiza pa ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu, Mulungu wake wa Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
nasunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi chimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asiriya, kulimbitsa manja ao mu ntchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho pa masiku asanu ndi awiri anasangalala pa chikondwerero cha buledi wopanda yisiti, chifukwa Yehova anawadzaza ndi chimwemwe. Iye anatembenuza mtima wa mfumu ya ku Asiriya motero kuti iyo inakomera mtima Aisraeli ndi kuwathandiza ntchito yomanga Nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
nasunga madyerero a mkate wopanda cotupitsa masiku asanu ndi awiri ndi cimwemwe; pakuti Yehova adawakondweretsa, nawatembenuzira mtima wa mfumu ya Asuri, kulimbitsa manja ao mu nchito ya nyumba ya Mulungu, Mulungu wa Israyeli.