Ezra 6:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ziŵiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara adaazitulutsa ku Yerusalemu kunka nazo ku Babiloni, zonsezo zibwezedwe, zipite ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Chilichonse chikabwezedwe pamalo pake m'Nyumba ya Mulunguyo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi zipangizo za golide ndi siliva za nyumba ya Mulungu, zimene anazitulutsa Nebukadinezara m'Kachisi ali ku Yerusalemu, nazitenga kunka nazo ku Babiloni, azibwezere, nabwere nazo ku Kachisi ali ku Yerusalemu, chilichonse ku malo ake; naziike m'nyumba ya Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ziwiya zagolide ndi zasiliva za ku Nyumba ya Mulungu zimene Nebukadinezara anatenga mʼNyumba ya Mulungu ku Yerusalemu kupita nazo ku Babuloni, zonsezi zibwezedwe ndipo zipite ku Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Chilichonse chikabwezedwe pamalo pake mʼNyumbayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi zipangizo za golidi ndi siliva za nyumba ya Mulungu, zimene anaziturutsa Nebukadinezara m'Kacisi ali ku Yerusalemu, nazitenga kumka nazo ku Babulo, azibwezere, nabwere nazo ku Kacisi ali ku Yerusalemu, ciri conse ku malo ace; naziike m'nyumba ya Mulungu.