Ezra 6:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuwonjezera pamenepo, ndikupanga lamulo lonena za m'mene mudzaŵachitire atsogoleri a Ayudawo zothandiza pomanganso Nyumbayo. Anthuwo muŵalipire msanga kuchokera m'thumba lachifumu, kuchotsa pa msonkho wa dera la Patsidya pa Yufurate.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndilamuliranso za ichi muzichitira akulu awa a Ayuda, kuti amange nyumba iyi ya Mulungu, ndiko kuti mutengeko chuma cha mfumu, ndicho msonkho wa tsidya la mtsinje, nimupereke zolipira kwa anthu awa msanga, angawachedwetse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kuwonjezera pamenepo, ndikukhazikitsa lamulo lonena za mmene mudzachitire ndi akuluakulu a Ayuda powathandiza kumanganso Nyumba ya Mulunguyo: Anthuwa muwalipire msanga kuchokera mʼthumba la ufumu, kuchotsa pa msonkho wa dera la Patsidya pa Yufurate.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndilamuliranso za ici muzicitira akuru awa a Ayuda, kuti amange nyumba iyi ya Mulungu, ndiko kuti mutengeko cuma ca mfumu, ndico msonkho wa tsidya la mtsinje, nimupereke zolipira kwa anthu awa msanga, angawacedwetse.