Ezra 7:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zitapita zaka zambiri, pamene Arita-kisereksesi anali mfumu ya ku Persiya, panali wansembe wina dzina lake Ezara. Iyeyu anali mdzukulu wa Aaroni, mkulu wa ansembe woyamba wa Israele. Makolo ake anali aŵa: Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Zitatha izi tsono, pokhala mfumu Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya, anadza Ezara mwana wa Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zitatha izi, Aritasasita ali mfumu ya ku Perisiya, panali wansembe wina dzina lake Ezara. Iyeyu abambo ake anali Seraya mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Zitatha izi tsono, pokhala mfumu Aritasasta mfumu ya Perisiya, anadza Ezara mwana wa Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,