Ezra 7:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano ndikupanga lamulo lakuti Mwisraele aliyense kapena ansembe ao, kapena Alevi okhala m'dziko mwanga, amene afuna kuti apite ku Yerusalemu mwaufulu, apite nawe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndilamulira kuti onse a ana a Israele, ndi ansembe ao, ndi Alevi, m'ufumu wanga, ofuna eni ake kumuka ku Yerusalemu, apite nawe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano ndikulamula kuti Mwisraeli aliyense, wansembe kapena Mlevi wokhala mʼdziko langa, amene akufuna kupita ku Yerusalemu ndi iwe, apite.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndilamulira kuti onse a ana a Israyeli, ndi ansembe ao, ndi Alevi, m'ufumu wanga, ofuna eni ace kumuka ku Yerusalemu, apite nawe.